Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 4:2 - Buku Lopatulika

ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iwoŵa anali okwiya chifukwa chakuti atumwi aŵiriwo ankaphunzitsa anthu ndi kulalika kuti, “Popeza kuti Yesu adauka kwa akufa, ndiye kuti akufa adzaukanso.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anakhumudwa kwambiri chifukwa atumwiwo amaphunzitsa anthu ndi kumalalikira za kuuka kwa akufa mwa Yesu.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 4:2
18 Mawu Ofanana  

Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.


Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo.


koma mau awa amodzi okha, amene ndinafuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.


kuti Khristu akamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu.


Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa?


ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.


Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa,


Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.


Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.