Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
Machitidwe a Atumwi 4:13 - Buku Lopatulika Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abwalo aja adazizwa poona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane, ndiponso podziŵa kuti anali anthu wamba, osaphunzira kwambiri. Apo adazindikira kuti anali anzake a Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu. |
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.
Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.
Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu!
Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.
Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;
Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.
Ndipo anali pamodzi nao, nalowa natuluka ku Yerusalemu, nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye;
koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;
zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.