Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Machitidwe a Atumwi 3:8 - Buku Lopatulika Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao mu Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adalumpha, naimirira, nayamba kuyenda, ndipo adaloŵa nao m'Nyumba ya Mulungu akuyenda ndi kulumpha ndi kutamanda Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu. |
Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.
Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo.
Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.
Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawagonjetsa onsewo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa.
Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa.