Machitidwe a Atumwi 3:5 - Buku Lopatulika Ndipo iye anavomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anavomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye nkuŵayang'anadi namaganiza kuti alandira kanthu kwa iwo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo. |
Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.