Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye.
Machitidwe a Atumwi 3:4 - Buku Lopatulika Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adampenyetsetsa, ndipo Petro adamuuza kuti, “Tatiyang'ana” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” |
Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye.
Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?
Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikulu pamenepo, ananena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi?
Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.
chimenecho ndidachipenyetsetsa ndinachilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zilombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.
Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai.
Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.
Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?