Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 3:2 - Buku Lopatulika

Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa mu Kachisi;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kachisi;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu ena adaanyamula munthu wina wopunduka miyendo chibadwire. Masiku onse ankamuika pa khomo la Nyumba ya Mulungu lotchedwa “Khomo Lokongola,” kuti iye azipempha kwa anthu oloŵa m'Nyumbamo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 3:2
9 Mawu Ofanana  

ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda,


Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha;


Chifukwa chake anzake ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha?


nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.


Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.


Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayende nthawi zonse.


namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Chipata Chokongola cha Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.


Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.