Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.
Machitidwe a Atumwi 3:11 - Buku Lopatulika Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu uja adaakangamira Petro ndi Yohane, ndipo anthu onse adadabwa, naŵathamangira ku Khonde lotchedwa Khonde la Solomoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni. |
Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.
Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena,
Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'chilankhulidwe chake cha iye yekha.
Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?
Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.