Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.
Machitidwe a Atumwi 27:2 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tidakwera chombo chochokera ku Adramitio chimene chinali chokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tidanyamuka. Aristariko, Mmasedoni wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tinakwera sitima ya pamadzi yochokera ku Adramutiyo imene inali yokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tinanyamuka. Aristariko, wa ku Makedoniya wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe. |
Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.
Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.
Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.
Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.
Ndipo m'mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.
Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;
Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,
Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.
Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.
Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye),