Machitidwe a Atumwi 26:1 - Buku Lopatulika Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Agripa adauza Paulo kuti, “Tikukulola kuti unene mau ako.” Tsono Paulo adatambalitsa dzanja lake nayamba kunena nkhani yake. Adati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Agripa anawuza Paulo kuti, “Takulola kuti unene mawu ako.” Paulo anatambasula dzanja lake nayamba kudziteteza kuti, |
Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;
Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana aakazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.
Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?
Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.
Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze.
Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;
Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;
Koma kwa Israele anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.