Machitidwe a Atumwi 24:4 - Buku Lopatulika Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pepani sindikufuna kukutayitsani nthaŵi, komabe ndimapempha kuti mundikomere mtima, mungomvapo mau athuŵa mwachidule. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma kuti tisakuchedwetseni, ndikupempha kuti mwa kuleza mtima kwanu mutimvere ife. |
Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;
ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso, monga ndinalemba kale mwachidule,
Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;