Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
Machitidwe a Atumwi 24:2 - Buku Lopatulika Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Pauloyo atamuitana, Tertulo uja adayambapo zomunenezazo. Adati, “Inu a Felikisi olemekezeka, ife tikukhala pa mtendere weniweni chifukwa cha inu, ndipo zinthu zambiri zakhala zikukonzeka m'dziko mwathu chifukwa cha utsogoleri wanu wanzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamuyitana Paulo, ndipo Tertuliyo anafotokozera Felike nkhani yonse ya Paulo. Iye anati, “Wolemekezeka, ife takhala pamtendere nthawi yayitali chifukwa cha inu, ndipo utsogoleri wanu wanzeru wabweretsa kusintha mʼdziko lino. |
Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.
Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.