Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
Machitidwe a Atumwi 20:2 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adayendera madera a komweko nalimbitsa mtima anthu ndi mau ambiri. Pambuyo pake adapita ku Grisi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayendera madera a kumeneko, nalimbitsa mtima anthu, ndipo pomaliza pake anapita ku Grisi. |
Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.
pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.
Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.
Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.
Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.
Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya.
Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kucha, anachokapo.
Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.
Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.
amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;
monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,
Pakuti kudandaulira kwathu sikuchokera kukusochera, kapena kuchidetso, kapena m'chinyengo;
Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.