Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.
Machitidwe a Atumwi 20:1 - Buku Lopatulika Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Phokoso lija litatha, Paulo adaitanitsa ophunzira aja, naŵalimbitsa mtima. Ndipo atatsazikana nawo, adachoka napita ku Masedoniya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Litatha phokoso, Paulo anayitanitsa ophunzira ndipo atawalimbikitsa anawatsanzika ndipo ananyamuka kupita ku Makedoniya. |
Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.
ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.
pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.
Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.
Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.
Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.
Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya.
mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;
Mupatsane moni wina ndi mnzake ndi kupsompsonana kopatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni.
Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.
Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,