Machitidwe a Atumwi 2:8 - Buku Lopatulika Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nanga bwanji aliyense mwa ife akuŵamva akulankhula chilankhulo chakwao? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo? |
Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?
Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.