Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Machitidwe a Atumwi 2:34 - Buku Lopatulika Pakuti Davide sanakwere Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Davide sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati, “ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti, “ ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti: Khala kudzanja langa lamanja |
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.
Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala mu Mwambayo.
ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo
Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?