Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
Machitidwe a Atumwi 2:26 - Buku Lopatulika mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m'manda, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera; thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo. |
Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola.
Pakuti Davide anena za Iye, Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse; chifukwa ali padzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;
Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,