Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
Machitidwe a Atumwi 19:3 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paulo adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono mudabatizidwa ndi ubatizo wotani?” Iwo adati, “Ndi ubatizo wa Yohane.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Paulo anawafunsa kuti, “Nanga munabatizidwa ndi ubatizo wotani?” Iwo anati, “Ubatizo wa Yohane.” |
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.
Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;
pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.
Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.
a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.