Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani.
Machitidwe a Atumwi 18:3 - Buku Lopatulika ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye popeza kuti iwo anali amisiri a ntchito imodzimodzi ngati yake, yosoka mahema, iyeyo adakhala nawo namagwirira limodzi ntchito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi. |
Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani.
ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira;
Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.
Koma ine sindinachite nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.
Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.
Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?
ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.
Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi.
Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.
ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;