Machitidwe a Atumwi 17:8 - Buku Lopatulika Ndipo anavuta anthu, ndi akulu a mzinda, pamene anamva zimenezi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anavuta anthu, ndi akulu a mudzi, pamene anamva zimenezi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mau ameneŵa adautsa mitima ya anthuwo ndi ya akulu amumzinda aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamva zimenezi, gulu la anthu ndi akulu a mzinda anavutika mu mtima. |
Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;
Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.
amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu.