Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Machitidwe a Atumwi 16:7 - Buku Lopatulika pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleze; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adafika ku malire a Misiya, adayesa kuloŵa m'dera la Bitiniya, koma Mzimu wa Yesu sadaŵalole. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero. |
Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!
Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;
Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya,
ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.