Machitidwe a Atumwi 16:4 - Buku Lopatulika Pamene anapita kupyola pamizinda, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ankadutsa m'mizinda, ankadziŵitsa anthu mfundo zimene atumwi ndi akulu a mpingo a ku Yerusalemu aja adaapanga, nkumaŵauza kuti azisunge. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene amayenda mzinda ndi mzinda, amafotokoza zimene atumwi ndi akulu ampingo ku Yerusalemu anagwirizana kuti anthu azitsatire. |
Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.
Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.