koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.
Machitidwe a Atumwi 16:3 - Buku Lopatulika Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Paulo adafuna kuti iye amperekeze. Tsono adamuumbala chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko, pakuti onse ankadziŵa kuti bambo wa Timoteo ndi Mgriki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki. |
koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.
Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.
Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhale ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;
(pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);
Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.
Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.