Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),
Machitidwe a Atumwi 16:2 - Buku Lopatulika Ameneyo anamchitira umboni wabwino abale a ku Listara ndi Ikonio. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ameneyo anamchitira umboni wabwino abale a ku Listara ndi Ikonio. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale a ku Listara ndi a ku Ikonio ankamtama Timoteoyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abale a ku Lusitra ndi Ikoniya anamuchitira iye umboni wabwino. |
Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),
Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira.
Pamene analalikira Uthenga Wabwino mumzindamo, nayesa ambiri ophunzira, anabwera ku Listara ndi Ikonio ndi Antiokeya,
iwo anamva, nathawira kumizinda ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:
Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.
Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.
Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.
Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.
wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.
Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.
mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.