Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 14:9 - Buku Lopatulika

Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iyeyo ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Paulo adampenyetsetsa, ndipo ataona kuti munthuyo ali ndi chikhulupiriro choti nkuchira,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 14:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri.


Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.


Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.


Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.


Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.


Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.


Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.


Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife.