Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.
Machitidwe a Atumwi 13:11 - Buku Lopatulika Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ona dzanja la Ambuye likukantha tsopano apa. Ukhala wakhungu osaonanso dzuŵa pa kanthaŵi.” Nthaŵi yomweyo khungu ndi mdima zidamgweradi, ndipo adayamba kufunafuna anthu oti amgwire dzanja ndi kumtsogolera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. |
Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.
Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti.
Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.
Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.
Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.
Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.
Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.
Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;
Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.
Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.
Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.