Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.
Machitidwe a Atumwi 13:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mu mpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi awa: Barnaba, Simeoni, Lukia wa ku Kurene, Manayeni (amene analeredwa pamodzi ndi mfumu Herode), ndiponso Saulo. |
Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake.
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;
Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.
Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.
Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe mu Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.
Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.
Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnabasi (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kipro,
Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,
Timoteo wantchito mnzanga akupatsani moni; ndi Lusio ndi Yasoni ndi Sosipatere, abale anga.
Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.
Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.
Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.
ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;