Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.
Machitidwe a Atumwi 11:8 - Buku Lopatulika Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ine ndidati, ‘Iyai pepani Ambuye, ine ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa sichinaloŵepo pakamwa pangapa.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndinayankha kuti, ‘Ayi, Ambuye! Pakuti chinthu chodetsedwa ndi chonyansa sindinadyepo pakamwa pangapa.’ |
Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.
ndi kuti musiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi pakati pa zodetsedwa ndi zoyera;
kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.
Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m'mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba.
Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.
Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.