Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo;
Machitidwe a Atumwi 11:5 - Buku Lopatulika Ndinali ine m'mzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ine ndinkapemphera m'mudzi wa Yopa. Ndidaachita ngati kukomoka, ndiye ndidaona ngati kutulo chinthu china chikutsika pansi kuchokera kumwamba. Chinkaoneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai, ndipo chidafika pamene panali ineyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndimapemphera mu mzinda wa Yopa ndipo ndili ngati wokomoka ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chokhala ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba chogwiridwa msonga zake zinayi, ndipo chinatsikira pa ine. |
Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo;
Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.
Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,
Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,
Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.
Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.