Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
Machitidwe a Atumwi 10:9 - Buku Lopatulika Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mzinda, Petro anakwera patsindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake, iwo aja akali m'njira koma akuyandikira mudziwo, Petro adakwera pa denga kukapemphera, nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera. |
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.
ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.
ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.
Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.
ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;
Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.