Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Machitidwe a Atumwi 10:8 - Buku Lopatulika ndipo m'mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo m'mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kornelio uja ataŵafotokozera zonse, adaŵatuma ku Yopa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawafotokozera zonse zimene zinachitika ndipo anawatuma kuti apite ku Yopa. |
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,
Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.
Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;
Koma mu Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.
Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.
Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.
kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi: