Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.
Machitidwe a Atumwi 10:6 - Buku Lopatulika acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akukhala kwa Simoni wina, mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye akukhala ndi Simoni mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.” |
Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.
Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja.
Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;
Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.