Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.
Machitidwe a Atumwi 10:10 - Buku Lopatulika koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ali pamenepo, adamva njala, namafuna kudya. Koma pamene anthu ankakonza chakudya, iye adachita ngati wakomoka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka. |
Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.
M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israele, nandikhalitsa paphiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mzinda kumwera.
anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.
wakumva mau a Mulungu anenetsa, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.
Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.
Ndinali ine m'mzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine;
Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,