Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
Machitidwe a Atumwi 1:4 - Buku Lopatulika ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adaŵalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina atasonkhana nawo pamodzi, Yesu analamulira ophunzira ake kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate anga analonjeza yomwe ndinakuwuzani. |
Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?
Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse,
Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.
Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.
si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.
Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.