Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.
Machitidwe a Atumwi 1:23 - Buku Lopatulika Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo iwo adatchula maina aŵiri: Yosefe amene ankamutcha Barsabasi (dzina lake lina ndi Yusto,) ndi Matiasi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi. |
Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.
Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.
Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo: