Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.
Machitidwe a Atumwi 1:22 - Buku Lopatulika kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuyambira pamene Iye adabatizidwa ndi Yohane mpaka tsiku limene adatengedwa kuchoka pakati pathu kupita Kumwamba. Mmodzi mwa anthu ameneŵa akhale mboni pamodzi ndi ife, yakuti Yesu adauka kwa akufa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.” |
Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.
Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.
Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,
amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.
kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;
Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.
tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;