Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Luka 9:8 - Buku Lopatulika koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kuti mneneri wina wa akale aja anauka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kuti mneneri wina wa akale aja anauka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ena ankanena kuti, “Iyai, ameneyu ndi Eliya, waonekanso.” Enanso ankati, “Iyai, koma ndi mmodzi mwa aneneri akale aja, wauka kwa akufa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso. |
Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?
Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya. Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo.
Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.
Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai.