Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndiyambe ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?
Luka 9:61 - Buku Lopatulika Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muyambe mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muthange mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu winanso adauza Yesu kuti, “Ndidzakutsatani, Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsazikana ndi anthu kunyumba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.” |
Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndiyambe ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.
ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.
amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu.