Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
Luka 9:57 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene iwo anali panjira, munthu wina adauza Yesu kuti, “Ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.” |
Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,
Petro ananena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu.