Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.
Luka 9:53 - Buku Lopatulika Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu am'mudzimo sadafune kumlandira, chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. |
Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.
Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.
Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).