Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.
Luka 9:40 - Buku Lopatulika Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.” |
Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.
Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.
Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.
ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.
Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.