Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.
Luka 9:34 - Buku Lopatulika Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akulankhula choncho, padafika mtambo nuŵaphimba, ndipo ophunzirawo adagwidwa ndi mantha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta. |
Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.
Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya aakuluwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi chimphamvu ine.
Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.
Ndipo munatuluka mau mumtambo, nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani Iye.
Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,
Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! Popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.