limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.
Luka 9:25 - Buku Lopatulika Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? |
limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
(Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;
alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.