ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Luka 9:22 - Buku Lopatulika nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adati, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma mkucha wake adzauka kwa akufa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.” |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.
Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.
koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.
Ndipo m'mene anali kutsotsa mu Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;
nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.
Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.
Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
ndi kunena, kuti, Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ochimwa, ndi kupachikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lachitatu.
ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.