Luka 9:21 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu aliyense; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu aliyense; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adalamula ophunzira ake kuti asauze munthu wina aliyense zimenezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi. |
Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.
Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.
Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense.