Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 9:13 - Buku Lopatulika

Koma anati kwa iwo, Muwapatse chakudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.” Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.”

Onani mutuwo



Luka 9:13
8 Mawu Ofanana  

Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno.


Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu.