Luka 8:7 - Buku Lopatulika Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nkuzitsamwitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. |
Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nkuzitsamwitsa, ndipo sizinabale zipatso.
Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;
Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.
Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho.
Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.