si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.
Luka 8:54 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adagwira mwanayo pa dzanja nanena mokweza mau kuti, “Mwana iwe, dzuka!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, “Mwana wanga, dzuka!” |
si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.
Koma pamene khamulo linatulutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka.
ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?
Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake.
Ndipo mzimu wake unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo Iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya.
Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.
Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.
monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.