Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.
Luka 8:53 - Buku Lopatulika Ndipo anamseka Iye pwepwete podziwa kuti anafa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamseka Iye pwepwete podziwa kuti anafa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola, chifukwa ankadziŵa kuti mwanayo wamwalira basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. |
Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.
ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.
Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.
Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.