Luka 8:51 - Buku Lopatulika Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu adafika kunyumba kuja, sadalole kuti wina aliyense aloŵe naye, koma Petro, Yohane ndi Yakobe, ndiponso bambo wake wa mwanayo ndi mai wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. |
Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.
Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo,
Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupirira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.
Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.
Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.
Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.