Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;
Luka 8:40 - Buku Lopatulika Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu adafikanso ku tsidya, chinamtindi cha anthu chidamchingamira, popeza kuti onse ankamudikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera. |
Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;
Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.
Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.
pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye.
Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;
Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumzinda wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye.
Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.
Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.